News

40 Million Kuchokera kwa Prophet Shepherd Bushiri

Akuluakulu a bungwe la Film Association of Malawi masana ano akukumana ndi mkulu wa Shepherd Bushiri Foundation, Prophet Shepherd Bushiri komwe mwazina apereka pempho la 50 million Kwacha.
Motsogozedwa ndi president wa bungweli, Dorothy Kingston, bungweli lapempha a Bushiri kuti awathandize ndi ndalamayi yomwe mwazina ndiku khazikitsa ofesi, kugula zipangizo zojambulira filimu komanso zochitika zina.
Koma bungweli lati likhala lokondwa ndi thandizo linalililonse lomwe a Bushiri angakwanitse ngati sangafikire pa 50 million-po.
Poyankhapo a Bushiri ati apereka 40 million Kwacha kuti awone momwe ndalamazi zigwilire ntchito yake, ndipo ngati gawo loyamba la ndalamali ligwire bwino ntchito, adzaperekanso gawo lomalizalo